Dziwani za matenda a Mpox
Mawu Oyamba
Unduna wa za Umoyo ukulengeza kuti kwadza matenda otchedwa Mpox omwe avuta m’mayiko ambiri ku m’mwera kwa Africa. Anthu ambiri adwala komanso kumwalira ndi matendawa. Bungwe la za Umoyo pa dziko lonse la World Health Organisation lidalengeza pa 14 August, 2024 kuti mliri wa matendawa tsopano ndi chiopsezo cha zaumoyo chokhudza maiko onse pa dziko la pansi.
Kulengezaku kudachitika potsatira kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu amene akupezeka ndi matendawa m’maiko ambiri
Kodi Mpox ndichiyani?
Mpox ndimatenda omwe amayamba ndi tizirombo tamtundu wa Vayirasi ndipo amafala pakati pa nyama za kutchire komanso anthu.
Mpox imafala bwanji?
Matendawa amafala pakati pa anthu kudzera mnjira izi:
• Kukhudzana ndi zilonda kapena zama
dzimadzi zochokera m’thupi la munthu
amene akudwala matendawa.
• Kukhudzana ndi zotuluka m’thupi
pamene odwala akupuma, kuyetsemula
kapena kutsokomola.
• Kukhudza zinthu zomwe zili ndi
tizirombo toyambitsa matendawa
monga zofunda, ziwiya kapena zovala.
• Kudya nyama kapena zinthu zina
zochokera kunyama zakutchire.
ziwani kuti kupita ku dera kumene matendawa abuka ndi china chomwe chingaikenso munthu pa chiopsezo chodwala matendawa.
Zizindikiro zake ndi ziti?
Zizindikiro za Mpox ndi izi;
• Kutentha thupi,
• Kutuluka matudza pa khungu,
• Kutuluka mwanabele,
• Kupweteka kwa mutu ndi Kufooka.
Ndani amene angadwale Mpox?
Aliyense akhoza kudwala Mpox koma amene ali pa chiopsezo chachikulu ndi magulu awa;
• Ana,
• Amayi oyembekezera,
• Amene ali ndi chitetezo cha mthupi chotsika,
• Azaumoyo,
• Amene akhudzana ndi munthu odwala matendawa
• Oyenda maulendo opita kapena kubwera ku mayiko omwe kuli matendawa.
• Anthu amene ali paubwenzi ndi kugonana ndi anthu ambirimbiri,
Tingapewe bwanji Mpox?
Titha kupewa Mpox potsatira izi:
• Popewa kudya nyama kapena zinthu zina
zochokera kunyama zosaphikidwa
mokwanira.
• Popewa kukhudzana ndi munthu yemwe
wapezeka ndi Mpox kapena zinthu
zimene zakhudzana ndi odwala monga
zovala ndi zofunda.
• Pogwiritsa ntchito mkati mwachigongono
cha dzanja lanu potsokomola kapena
kuyetsemula.
• Pewani kupita kudera komwe kwagwa
matendawa.
• Sambani m’manja ndi sopo pafupipafupi.
• Khalani motalikirana ndi anzanu
pamtunda osachepera 1 mita.
• Dziwitsani azaumoyo mwansanga ngati
mukumva kapena kuona zizindikiro za
matendawa
Kodi pali mankhwala ochiza Mpox?
Padakali pano palibe mankhwala enieni ovomerekezeka ochizira matenda a Mpox komabe mankhwala ena amathandiza kupewa zovuta zimene matendawa angabweretse kwa odwala.
Kodi pali katemera wa Mpox?
Katemera wa Mpox alipo. Katemerayu ndioyenera kuperekedwa kwa anthu amene ali pa chiopsezo chochuluka chodwala matendawa makamaka pamene matendawa abuka ku dera.
Kodi muchite chiyani ngati inu kapena wina ali ndi zizindikiro za Mpox?
• Pitani ku chipatala msanga kuti
mukalandire thandizo.
• Khalani modzipatula ndi anzanu ku¬kira
mutachira.
• Odwala matendawa akhale ndi ziwiya
zake zogwiritsira ntchito monga zofunda,
zosambira, zodyera ndi zovala.
Tikumbukire izi
Aliyense akhonza kudwala matenda a Mpox choncho ndikofunika tonse titsatire njira zopewera matendawa.
(Uthengawu wakonzedwa ndi a unduna wa zaumoyo)