Ana mukuwawona pa chitchunziwa ndi apa Lilongwe Social Rehabilitation Centre komwe Boma la Malawi mothandizana ndi bungwe la YONECO amapeleka chisamaliro kwa anawa.

Anawa lero atchena ma yunifomu aku sululu atsopano. Yunifomuzi ndi mphatso kuchokera kwa mayi Kaitano komanso mayi Chimwaza omwe ndi munthu ndi mkulu wake.

Mayi Chimwaza ali ndi shopu yosoka zovala ndipo kotero anawona kuti nkwabwino kuti asokokere anawa yunifomuzi.
Aka sikoyamba amayi awiriwa kuperekha thandizo kwa anawa. M’buyomu, mayi Kaitano omwe ali ndi malo odyera (restaurant) anapelekanso thandizo la chakudya akwa anawa.

Ambuye adalitse pomwe mayi Kaitano ndi mayi Chimwaza achotsa kuti afikire anawa.

0Shares

Leave a Comment